Song of Solomon 2

Mkazi

1Ine ndine duwa la ku Saroni,
duwa lokongola la ku zigwa.
Mwamuna

2Monga duwa lokongola pakati pa minga
ndi momwe alili wokondedwa wanga pakati pa atsikana.
Mkazi

3Monga mtengo wa apulosi pakati pa mitengo ya mʼnkhalango
ndi momwe alili bwenzi langa pakati pa anyamata.
Ndimakondwera kukhala pansi pa mthunzi wako,
ndipo chipatso chake ndi chokoma mʼkamwa mwanga.
4Iye wanditengera ku nyumba yaphwando,
ndipo mbendera yake yozika pa ine ndi chikondi.
5Undidyetse keke ya mphesa zowuma,
unditsitsimutse ndi ma apulosi,
pakuti chikondi chandifowoketsa.
6Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere,
ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.
7Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani
pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo:
Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa
mpaka pamene chifunire ichocho.

8Tamverani bwenzi langa!
Taonani! Uyu akubwera apayu,
akulumphalumpha pa mapiri,
akujowajowa pa zitunda.
9Bwenzi langa ali ngati gwape kapena mwana wa mbawala.
Taonani! Uyo wayima kuseri kwa khoma lathulo,
akusuzumira mʼmazenera,
akuyangʼana pa mpata wa zenera.
10Bwenzi langa anayankha ndipo anati kwa ine,
“Dzuka bwenzi langa,
wokongola wanga, ndipo tiye tizipita.
11Ona, nyengo yozizira yatha;
mvula yatha ndipo yapitiratu.
12Maluwa ayamba kuoneka pa dziko lapansi;
nthawi yoyimba yafika,
kulira kwa njiwa kukumveka
mʼdziko lathu.
13Mtengo wankhuyu ukubereka zipatso zake zoyambirira;
mitengo ya mpesa ya maluwa ikutulutsa fungo lake.
Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga
tiye tizipita.”
Mwamuna

14Nkhunda yanga yokhala mʼmingʼalu ya thanthwe,
mʼmalo obisala a mʼmbali mwa phiri,
onetsa nkhope yako,
nʼtamvako liwu lako;
pakuti liwu lako ndi lokoma,
ndipo nkhope yako ndi yokongola.
15Mutigwirire nkhandwe,
nkhandwe zingʼonozingʼono
zimene zikuwononga minda ya mpesa,
minda yathu ya mpesa imene yayamba maluwa.
Mkazi

16Bwenzi langa ndi wangadi ndipo ine ndine wake;
amadyetsa gulu lake la ziweto pakati pa maluwa okongola.
17Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira
ndipo mithunzi ikayamba kuthawa,
unyamuke bwenzi langa,
ndipo ukhale ngati gwape
kapena ngati mwana wa mbawala
pakati pa mapiri azigwembezigwembe.
Copyright information for NyaCCL